15/06/2026
THE MANIPULATED QUEEN
Chapter 128
Onse anali atakhala pasi koma akumuyang'ana Stella uja. Ana okha ndi amene anasazika nkumapita kukagona.
"Mother you could have told us. Osati kutizizimutsa."
"As if mukanakhulupila." Anatero Lydia. Anali atawafotokozera chilichonse mene zinthu zinakhalila.
Ena anali ndimafuso koma anangosankha kukhala chete.
"How can you fake your death Stella? Tinayendesa mwambo onse yet you were alive and breathing?"
Stella anawayang'ana ankolo ake amene amawoneka kuti anali atayamba kukalamba.
"I had no choice. "
"What do you mean ukamati panalibe choice!"
"Don't shout."
"Why shouldn't I? Now aliyense aziti wauka kwa akufa. Mwambo unachita kuyendesedwa. And everyone saw everything. "
"I will clear everything out. Ndikati I had no choice. I really did."
"Ndimadziwa kuti utha kupanga zinthu zonse koma osti kutipusisa akulu akulu ife."
"She said she had no choice. Ndiye ukufuna kuti afotokoze chani? And wanena kuti apanga explain chilichonse so live it like that." Lydia..
"Ndife akulu akulu. She was not supposed to do this to us."....
Pamene masiku a will anali atadusa Solo anayamba kumakwanisa kumva thupi lake mosiyana ndi mwanthawi zonse.
Anali atachosedwa kunyumba imene ankakhala ndi Jessica koma akukhala ndi Arena.
Arena anali atakhala pa mpando akumuyang'ana Solo uja.
"Ukuziwa sindikuziwa kuti what happened to you." Anatero akumuyang'ana nchimwene wake mwachidi.
"One day you were fine the next day wagwidwa ndi stroke. What happened brother? Whom did you wrong? Because it doesn't make sense." Anatero kenako anapumira mwamba.
Solo anasuntha mwendo koma Arena sanawone koma Solo anali atawona. Anayeseranso kuti asunthe mwedo wake koma zinakanika.
"Anyway, am here to tell you about your divorce. It was successful. Jessica anapempha zinthu zingapo. Ndinakumana ndi sister wake and we finalized everything...."
Anakhala kanthawi ngati akuganizira.
"You know am happy kuti wasiyana naye but am sad kuti uli chonchi. Don't worry your niece akabwera azikuchezesa. Ndikukhulupilira kuti lero sukulu akuonako kuchedwa kuti aweluke. She loves you. She really dose."
"Are.......na"
Arena anayang'ana chipinda modabwa ndipamene amazamuyang'ana Solo.
"Did you just speak?"
Solo anamuyang’ana.
"You said my name. I believe I heard you."
"Are...."
"Solo!"
Anagwira pakamwa ngati alili.
"You are speaking!"
"Na..."
Anayesera kusuntha thupi lake ndipo zinatheka.
"Solo!"
Anatuluka nchipinda muja mwachangu. Anakatenga foni yake nkuwayimbira adokotala kenako anayimbila bambo ake.
Pamene bambo ake amafika nkuti dokotala atafika kale akumupanga check Solo uja.
"Zikuonetsa kuti pali kusintha kwa mankhala amene amapasidwa and akuonetsa kuti mankhwala amenewo ndiamene akumuthandiza."
"Ndiye bwanji mbuyo monsemu samapasidwa?" Anafusa bambo ake.
"Chifukwa some medicine can react negatively to someone but positively to others and at the same time others are neutral they don't show any sighn. Mankhwala amene amapasidwa ndi amene akhala akuthandiza anthu osiyanasiyana koma to him zinali zovuta."
"Chabwino doctor. Koma akhala bwino?"
"He will surely be fine. "
"Ndimankhala amenewa. Zitenga nthawi yayitali bwanji?"
"2 to 3 weeks kuti akwanitse kulankhula. Adding to that azipita kokawawongola."
"He does that."
"Then kwinako sizivuta. Ngati zatheka kulankhula after 2 days. Kwinako sizivuta."
"Okay."
"I have to go. Kwinako azimalizisa nurse uja."
"Tathokoza doctor."
A doctor ananyamuka nkumapita.
Arena ndi bambo ake anamuyang’ana Solo.
"You will be fine son."
"Yes he surely will."....
Mbali ina Molly zinthu zinkamuyendera kwambiri.
Kulumikizana kwa iye ndi Zack kunafika pokoma kwambiri moti amamuza chilichonse. Mene siku lake layendela komanso antchuto amene anamukwiyisa.
Tsiku lina Zack anamutengera kunyanja koma dela limene kunalibe anthu ambiri.
Anakakwera boti limene mumakwera anthu atatu. Iwo ndi driver oyendesa. Dzuwa linali likuwala nthawiyo nkuti boti lija likuyenda pakati pa nyanja.
Anali atayima mphepete mwa boti kwinako Zack akumunong'oneza Molly.
Molly anaseka kenako analoza nsomba imene anayiwona.
"You are silly. Ukukuwa ngati nsoba sunaiwonepo bwanji?"
"Isn't it cute? Sindinaonepo nsomba ikusambira."
"Do you think ikusambira?"
"Ndiye ikutani?"
"Ikuyenda."
"No ikusambira mesa ili madzi."
"Madzi ndi media yake kaya."
"Koma madzi timatani mesa timasambila."
"Chabwino Chabwino eya ikusambira."
"Ndiye bwanji umanditsutsa?"
Zack anayima kumbuyo kwake.
"Ndi ngatsutse the mighty queen?"
"Am the queen now?"
"Yes of my heart, my head, my body in fact everything."
"That's sweet of you."
"Yes."
Anapitiliza kukamba nkhani zawo kwinako akumalozeraba zinthu.
Comment....