21/08/2026
Nduna yaza migodi a Thoko Tembo ati kusowa kwazipangizo zapamwamba zokumbila golide pakati pa magulu ochita za migodi ndi vuto lalikulu lomwe likuchitisa kuti magulu-wa azikanika kukumba golide wochuluka.
A Tembo ananena izi atayendela gulu la Nanjiri Mining Cooperative mdera la fumu yayikulu Chadza m'boma la Lilongwe.
Iwo ati boma layamba kale kukambilana ndi mabank ndi ma bungwe ena kuti athandize mabungwewa ndicholinga choti apeze zipangizo zapamwamba.
Ndipo Mkulu wa gulu Nanjiri Mining Cooperative a Stanley Yolamu apempha boma kuti liyambe kupelekaso ziphanso zopangila ntchito migodi ndi cholinga choti azigwira ntchito zawo mwa mtendere.
Dziko la Malawi likutaya ndalama zochuluka $700 million (Zomwe ndipafupifupi MK 1.2 billion) pa chaka zomwe anthu akumagulisa golide modzembela boma.