04/07/2025
Patapita zaka zochuluka aMalawi akusowa mtengo ogwira ndi nthenda ya Khansa kamba koti dziko lino linalibe chipatala chakechake cha nthendayi, utsogoleri wa Pulezidenti *Lazarus Chakwera,* wakwanitsa kumanga chipatala cha nthendayi mu mzinda wa Lilongwe.
Chipatalachi chatsekulidwa lachitatu pa 2 Julayi, 2025, ndipo Mtsogoleri wa dziko lino ndamene watsekulira.
Polankhula atatsekulira chipatalachi, Mtsogoleri wa dziko lino anati kwa zaka zambiri dziko la Malawi lataya anthu ochuluka kamba ka nthenda ya Khansa, omwe akanathandiza pa chitukuko cha dziko.
"Mchifukwa chake nditasankhidwa kukhala Mtsogoleri wa dziko, ndinalingalira kuti ndi ndani amene ndingamufikire kuti andithandize kumanga chipatala cha Khansa, njira zonse zitawoneka kuti zakanika ngakhale nthawi imene ndinali mnyumba ya Malamuro ngati phungu kuyesayesa kupeza mayankho othanirana ndi nthendayi" Anatero Mtsogoleri wa dziko lino.
Koma Pulezidenti Chakwera wati ndiwokondwa tsopano kuti anthu odwala nthenda ya Khansa ali ndi chiyembekezo kamba kakumangidwa kwa chipatala chamakonochi mdziko muno.
Chipatala cha Khansa chomwe chamangidwa mu mzinda wa Lilongwe, ndipo ndi choyamba kumangidwa pansi pa boma mdziko muno, chinayambika mchaka cha 2022 ndi masomphenya a Pulezidenti Chakwera.
@ *_Chilimunthaka_*