01/09/2025
๐๏ธ 1 Sept, 2025
Kadzutsa wa Mau, ULENDO OWERENGA BIBLE
๐ Numeri 21:1-35
๐ Ndime yolingalira: 8
*"Pamenepo Yehova Anati kwa Mose, Upange njoka yamoto; nuiike pa mtengo wake; ndipo kudzali, kuti onse olumwa, akuipenya njokayo, adzakhala ndi moyo."*
Muli mphamvu mu kupenyetsetsa!
Njoka za poison wakupha, zikulanga apaulendo ong'ung'udza, amwano ndi oderera!
"Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Aigupto kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu." (v 5)
Mana, chakudya cha angelo, lero akuyesedwa "mkate wachabe!" Zoona? Kung'ung'udza, kusayamika kumachititsa maso khungu! Munthu sazindikira kuya kwa madalitso omwe ali nao. Mana amaoneka ngati "mkate wachabe!"
KOMA taonani chisomo nanga! Wolumidwa asanafe, akukhala ndi mwayi woyang'anitsitsa pa njoka yamkuwa, yomwe Mulungu wauza Mose kupanga, nayikweza pa mtengo. "Yense wopenyetsetsa njokayo, nakhalanso ndi moyo."
Lero, monga zidaliri m'chipululu, Mulungu sakuchotsa njoka zaululu, zoluma, KOMA Akupereka njira ya chipulumutso kwa olumidwa; kukhala ndi moyo poyang'anitsitsa pa mtanda wa Yesu, kuti apeze moyo.
N'kutheka, inu ndi ine takhala amphulupulu, ong'ung'udza, amwano mu njirayi, pa ulendo wa m'zipululu za moyo uno! Chotiyenera ndi kulumwa ndi njoka, ndi kufa! Komatu chisomo chiripo poyang'anitsitsa pa Calvary, pomwe pali moyo wosatha mwa Yesu.
Monga Mulungu Adakhululukira Israyeli, nakhala "Thandizo lopezekeratu m'masautso" pa nkhondo zao, Mulungu Akhalenso thandizo lathu.
Israyeli wolumidwayo atayang'anitsitsa pa njoka ya mkuwa, adalanda dziko la Aamori (vs. 24 & 25) nagonjetsanso dziko la Basana (v. 35)
Kulumwa si mathero a nkhani, okondedwa! Yehova atha kutimenyera ife nkhondo zathu posakumbukira machimo omwe tavomereza ndi kuwasiya. Iye adzatipatsa chigonjetso tikapenyetsetsa pa Yesu.
Okondedwa, tiferenji chisomo chiripo? "Yang'ana pa mtanda kwa Yesuyo, kuti upeze moyowo... ๐ถ๐ต