Mangochi District Council

Mangochi District Council Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Mangochi District Council, Government Organization, Private Bag 138, Mangochi.

This is the Official page for Mangochi District Council, where updates on developmental projects and initiatives by the council, as well as development partners, are shared

Wachiwiri kwa Nduna yowona za chilengedwe a Chipiliro Mpinganjira yapeleka ndalama zokwana K500,000 kwa Duwana Muhammad ...
18/08/2026

Wachiwiri kwa Nduna yowona za chilengedwe a Chipiliro Mpinganjira yapeleka ndalama zokwana K500,000 kwa Duwana Muhammad kaamba ka mbiri yake ya maphunziro yomwe yalimbikitsa achinyamata ndi anthu ena.

Naye mkulu wa bungwe la Malawi Bureau of Standards a Symon Mandala sanachitire mwina koma kupeleka ina K500,000 kwa Duwana kaamba ka nkhani yake yomwe inawakhuza.

Izitu sizinathere p***a, pomwe mlembi mu unduna owona za masewero a Jasmeson Ndalama apeleka ndalama ina yokwana K200,000.

Pakadali pano mkulu wa Banki ya Standard a Philip Madinga alonjeza Duwana kuti amutsegulira akaunti ya maphunziro yomwe izisunga ndalamayi.

Izi zachitika lero, pa msonkhano wokambilana za a chinyamata *National Youth Summit* ku Lilongwe.

(Copied: Malawi).

16/08/2026

🎓 Official Maranatha Academy Page
✨ Home of Excellence& Character
📚 Admissions |Scholarships |Student Life
🌍 Raising Future Leaders• Learning
📍Malawi| Meliora Sequamur

*MWADZUKA BWANJI*!!!*M'mawa wa Lero Lachisanu, 14 August:*  Mangochi Boma kwacha ndi mitambo, ndi mvula ya mawawa. A zan...
14/08/2026

*MWADZUKA BWANJI*!!!

*M'mawa wa Lero Lachisanu, 14 August:* Mangochi Boma kwacha ndi mitambo, ndi mvula ya mawawa.

A zanyengo akuti Masanawa kutuluka dzuwa, ndipo
Kutentha kwambiri ndi 24°C.



Kumeneko kwacha bwanji?

*Tiyeni tikatipule*

District Council

KUTELESYE
13/08/2026

KUTELESYE

KUSAWISYE
13/08/2026

KUSAWISYE

12/08/2026
MAWA! MAWA! MAWA!  Pa 13 August, 2026,Tikumane ku Mangochi Stadium, komwe kuli mwambo wokweza mafumu: â—Ź A Wasi Mponda ku...
12/08/2026

MAWA! MAWA! MAWA! Pa 13 August, 2026,

Tikumane ku Mangochi Stadium, komwe kuli mwambo wokweza mafumu:

â—Ź A Wasi Mponda kukhala *ST/A KAPICHI*

â—Ź A Mtalika Kusala Friday kukhala *ST/A CHIPONDE*

Nthawi : Kuyambila 9 Kololo m'mawa.

Mlendo wolemekezeka pa mwambowu ndi Nduna ya Maboma ang'ono ang'ono, Dr. Ben Malunga Phiri.

Magule, ndi zina zambiriiiii zodyetsela maso zikakhalako.

Tiyeni tooooonse!!!!!!!!!!!!!!!!!

District Council

08/08/2026
Ofesi ya zaumoyo kuno ku Mangochi ikudziwitsa anthu onse kuti ipeleka  katemera  wa Poliyo owonjezera, kwa ana osaposera...
06/08/2026

Ofesi ya zaumoyo kuno ku Mangochi ikudziwitsa anthu onse kuti ipeleka katemera wa Poliyo owonjezera, kwa ana osaposera zaka 10, kuyambila pa 11 August mpaka pa 14 August chaka chino.

District Council

wa ana

KHONSOLO YA MANGOCHI YALANDIRA K2.8 BILLION YA CHITUKUKO PAKUPAMBANA MU UTSOGOLERI WABWINOKhonsolo ya Mangochi yalandira...
31/07/2026

KHONSOLO YA MANGOCHI YALANDIRA K2.8 BILLION YA CHITUKUKO PAKUPAMBANA MU UTSOGOLERI WABWINO

Khonsolo ya Mangochi yalandira ndalama zoposera K 2.8 billion kudzera mu pulogalamu ya Governance to Enable Service Delivery (GESD), kutsatila kupambana kwake pa utsogoleri wa bwino, kakonzedwe ka mapulani, komanso kuyendetsa bwino ndalama, mwa zina ( Local Authority Performance Assessment) pa chingelezi.

Izi zadziwika pa mwambo wolengeza m'mene Makhonsolo agwilira ntchito chaka changothachi, womwe nduna ya maboma an'gono an'gono, a Ben Phiri, komanso ya zachuma a Joseph Mwanamveka anachititsa ndi akulu akulu a m'makhonsolo, lero pa 31st July.

Kwa ma Khonsolo 28, Khonsolo ya Mangochi yakhala nambala 7 mu ndondomekoyi.

Pa mwambowu, Khonsolo ya Mangochi yalandilanso ndalama zoposa K628 Million za chitukuko, mu thumba lotchedwa RCRP-2.

Mmawu awo, Bwanankubwa wa Boma la Mangochi a Rodney Simwaka ati ndalamazi zithandiza kubweletsa zitukuko zochuluka m'madera a ku Mangochi.

"Ngati Khonsolo, ndife okondwa kuti talandila ndalama za nkhaninkhani mu thumba la GESD, zomwe zitithandizile kumanga zitukuko zosiyanasiyana m'magawo monga a maphunzilo, zaumoyo, za ulimi, ndi zina."

"Ine ngati Bwanankubwa, ndikhala patsogolo kuonetsetsa kuti ndalama izi zikugwila ntchito yake moyenera, ndipo pofuna kubweletsa chilungamo, tikhala ndi 'dashboard' ku ofesi kwathu, yomwe idziwonetsa mmene ndalamazi zikugwilira ntchito," atelo a Simwaka.

Iwo ati awonetsetsanso kuti Khonsolo ya Mangochi ikupitilira kupambana kuposela apa.

District Council

Ku Makhonsolo

# GESD

Address

Private Bag 138
Mangochi

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mangochi District Council posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share