07/08/2026
DPP RSA:
Mu ndale, mpikisano usakhale chifukwa chodana. M’malo mwake, ukhale mwayi wophunzira, kugwirizana ndikutumikira dziko.
Ndizosangalatsa kuona atsogoleri achinyamata akuwonetsa kuti mgwirizano ndi kukhulupirirana zingabweretse zotsatira zabwino. Tikamaona Hon. Leonard Chimbanga, First Secretary ku Malawi High Commission ku Pretoria, ndi Hon. Minister of Youth Sports & Culture-Hon Alfred Gangata,MP akugwira ntchito mwaulemu komanso mogwirizana pa maudindo awo, zimatiphunzitsa kuti ulemu, kulumikizana ndi mgwirizano ndizofunika kwambiri pa utsogoleri.
Achinyamata andale tiyeni tiphunzire kuti kupambana sikumachokera pa kunyozana koma pa kugwira ntchito limodzi, kulemekezana, komanso kuthandizana kuti dziko lipite patsogolo.
Tikakhala ogwirizana, timakhala amphamvu. Tikamakhulupirirana, timatha kukwaniritsa zolinga zazikulu.
Dziko limamangidwa ndi anthu omwe amasankha mgwirizano osati mikangano.
President Arthur Peter Mutharika akugwira ntchito yosula achinyama kuti azakhale atsogoleri a mawa.
Tiyeni achinyamata titengerepo phunziro.
Democratic Progressive Party - DPP