Christina Stories

Christina Stories Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Christina Stories, Library, Blantyre.
(1)

05/01/2026

After chi long time

29/01/2025

Koma mwaswera

13/10/2024

MISS YOU FAMILY

NDIKUBWERA POMPANO MUCHIMAKE

30/09/2024

MA BUSY KAYA KUMAYAMBILA PATI APA 😅

29/09/2024

Happy Sunday

BEHIND THE MIRRORCHAPTER 5" Nanga mamuna wako ngati wachoka koyendetsa galimoto ndikuyamba yotutira mchenga sikuvutika?....
20/08/2024

BEHIND THE MIRROR

CHAPTER 5

" Nanga mamuna wako ngati wachoka koyendetsa galimoto ndikuyamba yotutira mchenga sikuvutika?.komanso m'mene wakutengera muja mukungokhalabe nka nyumba kothinana chonchi anthu atatu, mukuchita kukanika kupeza nyumba yanu yanu yoti ndikumakhala panokha apa ndinkakuuzatu koma ine apa ndiye mudzingokhalira kuvutikaku".

"Kodi wangobwera kuno kumadzandinyoza si choncho? ". Anafunsa Brenda.
" Sikuti ndikukunyoza koma ukuyenera kutseguka m'maso ; tangodziona wekha m'mene ukuonekeramu zoti uli pa banja sizikuoneka chifukwa chosowa chithandizo".
"Ukudziwa chani Brenda sindili mood ya zomwe waziyambazi ndiye utha kunyamuka udzipita".
" Kusonyeza kuti ukundithamangitsa kwanu kuno? ".
" Ndi m'mene wamveramo ndithu nyamukani".

Ngati bodza Emily ananyamukadi kumapita kwawo kumusiya.

*PATATHA ZAKA ZIWIRI*

Brenda anali akukonza chakudya cha m'mawa , anali kukonza chakudyacho uku akumvera nyimbo.

Mamuna wake, Charles anabwera ndikudzamugwira mchiuno.
"Morning beautiful, walawira kaletu kununkhiritsa m'mawa uno".Anali kuyankhula Charles uku akufuna kumupsopsona Brenda.
Naye Brenda anamukumbatiranso Mamuna wakeyo ndikuyamba kupsopsonana awiriwo.

Anatenga nthawi akupsopsonana.
" Eeee basi hun ndisiye paja iwe ukayamba ndi mpaka ndichita kupseleletsa nazo chakudya apa".
"Ukukhala ngati nawe sumafuna bwanji, mwana wakonso akumveka kuti wadzuka apa ndipite ndikamutenge".

Charles anachoka pamalopa ndikupita kukamutenga Destiny kumusiya Brenda akukonzabe chakudya chija. Atamaliza kukonza chakudya chija Brenda anapita kukamusambitsa Destiny. apa nkuti Charles anali atangokhala kumamudikilira Mkazi wakeyo.

" Hun utha kuyamba kudyatu ndimudyetse kaye phala uyu". Anayankhula Brenda.
"Aaaa ndidya bwanji ndekha iwe ulipo ndikudikira basi".
" Komatu ndiye ikuwawatu".
"Aaaa zilibe ntchito zimenezo".

Charles anaumilira kumudikilira mkazi wakeyo kuti adye limodzi chakudyacho. Brenda atamaliza anakadyeradi limodzi chakudyacho akukamba nkhani zawo. Atamaliza Brenda anatenga mbale zomwe anagwiritsa ntchito zo ndikupita kukazitsuka.

Phone ya Brenda inayamba kuyitana, uyutu anali Emily, nzake wa Brenda uja. Charles anayitenga phone ija ndikupita nayo komwe kunali mkazi wakeyo.
" Hun, phone yako ikuyitanatu iyi". Anatero Charles akumupatsira Phone mkazi wakeyo.
"Akuyimba ndindaninso abale? ".
" Emily tu uyu mwina akufuna akuuze kuti wafika".

Brenda anayitenga phone ija ndikuyiyankha.
"Hello adona, ndafikatu". Anayankhula Emily pa phone paja.
" Chabwino ndiye ungokhala pa bus depot pompo abwera bambo a Destiny adzakutenga". Anayankhula Brenda.
"Chabwino". Anayankha Emily phone ija nkuduka.

"Mumanena zooona tu, ati wafika uyu mesa mupita mukamutenga". Anayankhula Brenda.
" Aaaa tipita limodzi nanga iweyo ukhala ukutani m'buyomu".
"Hmmmm mwatero ndiye ndingomaliza ichichitu nanga sindingachisiye chonchitu".
Brenda atamaliza zomwe anali kupangazo ananyamuka anthuwa ndikukakwera galimoto ulendo waku bus depot kukamutenga Emily. Anayenda njira yonse mpaka anakafika ku bus depot ko.

Emily anali atangoyima kudikilira kuti adzatengedwe. Brenda anali atamuzindikira Emily yo.
" Uyotu wayima apoyo". Anayankhula Brenda.
"Eya ndamuwona".
Charles anakayimitsadi galimoto yake pomwe panali Emily po.
" Emily". Anayitana Brenda mwansangala.
"Aaaa ndiinu kodi sindinakuzindikirenitu".Anayankhula Emily.
" Pajatu iwe bodza, bwerani mudzakwere tidzipitatu" Anayankhula Brenda.

Emily anabweradi pa galimoto po ndikudzakwera.
"Pepatu takudikiritsa". Anayankhula Brenda yo.
" Aaaa palibe vuto osadandaula".

"Mula muli bwanji? ". Anayankhula Charles.
" Inetu ndili bwino kaya inuyo".
"Ndili bwinonso, si basi tidzipita apa".
" Eya tiyeni". Anayankha Brenda.

Mu njira anthuwa anali kukamba nkhani zawo nkumaseka. Koma Emily maso ake onse anali pa Charles. Nkumuona kokha zinali kuonetseratu kuti anali atayamba kumusilira mamuna wa nzakeyo.

Atafika kwawo kwa Brenda, Chales sanachedwe nkucheza komwe phone yake inayitana. Anayitenga nkuyiyankha phone ija.
"Bwana, kwabwera anthu kuno oti akufuna mudzakambirane nanu nokha".
" Chabwino ndifika kumeneko pompano".

"Ndiye mula inutu bakachezani, ena andiyimbira phone apa ndikufunikiranso malo ena ake ndiye mwina ndikupezani". Anayankhula Charles akutenga ma key a galimoto.
" Aaaaa inutu tidzaonana chifukwa ulendowu ndi wa lero lomwe".Anayankhula Emily.
"Oh chabwino ndiye muyenda bwinotu".
" Zikomo ".
" Hun ndikupezatu". Anali kuyankhula Charles akumukumbatira mkazi wakeyo kenaka anamupsopsona pa mphumi Brenda yo..Zomwe anali kupanga awiriwa zinali kungomunyansa Emily yo koma sanakanena.

Charles anali kutuluka m'nyumbamu,naye Emily anali kungomuyang'anitsitsa mamuna wa nzakeyo. Brenda ataona kuti nzakeyo akumuyang'ana kwambirii mamuna wakeyo ananamizira kukhosomola.Izi zinapangitsa kuti nzakeyo asiye kumuyang'ana Charles yo.Naye Charles anakakwera galimoto ndikumapita komwe anali kupitako.

"Udzimuonako uyu kuzunguza ndikakukonzere chakudya". Anayankhula Brenda ndikuchokapo pamalopa. Atamaliza kukonza chakudyacho anampatsa Emily uja ndikuyamba kudya.
" Akulatu anyamata, bwanji sanayambe kupita ku school? ".
" Aaaa akadali wan'gono uyu sindingakamupatse ntchitoo munthu pamene ine ndikungokhala pano, adzapitabe akadzayamba kupanga chilichosee yekha monga kudziwa yekha nthawi yopita ku chimbudzi". Anayankhula Brenda.

Awiriwa anapitiriza kumakamba nkhani zina.
"Komano Brenda umakhala naye bwanji mamuna wakoyu? ". Anafunsa Emily.
" Kukhala?, ukutanthauza chani ukati kukhala".
"Aaa ndingoti umamuona bwanji mamuna wakoyu".
" kodi ukutanthauza chani iwe".
"Ndikutanthauza panopa m'mene analemeramu, mukumakhala bwanji ine ndikuona ngati m'mene munafika apapa ndiye kuti ali ndi akazi ena kunjako moti chikondi chonse akumakuonetserachi ndi cha bodza akungofuna akutchinge m'maso cholinga usazindikire zomwe amapanga kuseliko. Uyuyu si mamuna wabwino kuli bwino ungomusiya nthawi ikadalipo chifukwa adzakusiya mwa chipongwe. Taona mwinanso apapa m'mene wachokamu akukakomana ndi akazi ena, akuchita kuonekeratu kuti amapanga zoipa kuseli kwako ameneyu".

Ikupitilira.........

17/08/2024

SINDINAKUIWALENI

BEHIND THE MIRRORCHAPTER 4*PATATHA MASIKU ANGAPO*Charles anali kuyendetsa tax atakweza anthu, ali nkuyendetsa choncho ku...
15/08/2024

BEHIND THE MIRROR

CHAPTER 4

*PATATHA MASIKU ANGAPO*

Charles anali kuyendetsa tax atakweza anthu, ali nkuyendetsa choncho kutsogolo kwake kunali kudutsa mwana, koma zinali kuonetsa kuti mwanayo sanali kuona kuti kutsogolo kwake kuli kubwera galimoto, anayesa kuimba hutar koma mwanayo sanali kupatuka. Charles pofuna kuti asamugunde mwanayo ankapanga zoti ayikhotetse galimoto ija koma kwatsoka zinapezeka kuti galimoto ija inaluza ma break ndikukamenya mtengo wina omwe unali pamenepo ndipo galimotoyo inaphwanyika kutsogolo koma anthu onse anali bwino bwino opanda ovulala.

"Apa ndiye zanga zayipa basi nanga ndiyambira pati kuwauza abwana za galimotoyi". Anali kudziyankhulira yekha Charles kenaka anatenga phone yake ndikuwayimbira abwana ake.

" Wati zakhala bwanji?, wawononganso galimoto yanga kachikena? ".
" Koma bwana inali ngozi chabe".
"Ngozi, ngozi chani sumasamala kayendetsedwe kako ndipo undidikire pomwe ulipo ndikubwera konko". Anayankhula a bwana ake a Charles aja ndikudula phone ija.

Charles anakhala kumadikira abwana ake ndipo posakhalitsa anafika pa malopa. Anakambirana ndi abwana akewo.
" Ukudziwa chani akaka sikoyamba izizi zitachitika ndiye ndatopa ndikumangokonzetsa galimoto yanga chifukwa cha kusasamala kayendedwetsedwe kako, ndiye ndapanga chisankho choti mungosiya ntchito akakhala malipiro ako sindikupatsanso ndikunzetsere galimoto yangayi".
"Koma bwana mukanandimverako chisoni ; simungangondichotsa ntchito chonchi".
" Kukumvera chisoni kwake kukhale motani ndakuuza kale ndipo ukudziwanso kuti sindingasinthe maganizo anga utha kunyamuka".

Charles anayesera kuwanyengelera abwana ake aja koma sanamumvere ndipo anawuyamba obwelera komwe iye adali kukhala. Atafika kwawo adamupeza Brenda atangogona pakhonde, naye anafika nkukhala pomwepo. Kubwera kwa Charles kunamupangitsa kuti Brenda adzuke apatu nkuti nzake Felix atachokako naye atapita ku ntchito.

"Aaa wabwera kale nthawi ino,bwanji ma customer kulibe? , nanga nkhope yo yatani?, chachitika ndi chani? ". Anafikira kufunsa Brenda.
" Aaaa zinthu zake, ndinapanga ngozi ndiye galimoto yaonongeka, nditawadziwitsa abwana andichotsa ntchito ndipo sanandipatsenso malipiro".
"Komano kwenikweni chikuchitika ndichani?.. osadandaula koma mamuna wanga zonse zikhala bwino ndipo ntchito ina uyipeza". Anayankhula Momulimbikitsa Brenda.
" Eya komano nkhawa zanga ndizakuti timayenera kuchoka pakhomo pano ndikumakakhala patokha apapa m'malo moti tikanasintha nyengo ndi pamene mavuto akutiunjikiranso sindikudziwa kuti ndikamuuuza Felix zidzamumvekera bwanji ".
" Eya ndikudziwa komano ndikukhulupilira ziyenda tili limodzi usadandaule".

Madzulo ake Felix atabwera anamupeza Charles akuchezabe ndi Brenda pakhonde paja. Iye anali odabwa kumuona nzakeyo atabwera mofulumira choncho chifukwa nthawi zambiri anali kuyamba kufika amakhala Felix yo.

"Aaa man Charlie mwabwera kale ku ntchito nthawi ino chachitika ndi chani, kapena mwangobwerako mothawa yanu ija? ". Anafunsa Felix.
" Eya man zovutatu kutereku ndi zomwenso ndimakudikira kuti ndidzakuuzenso apa".
"Aaa chachitikanso ndi chani? ".
" Kungoti..... ".Anaima kaye kuyankhulako Charles ndikumuyang'ana Brenda, apatu Brenda yo anangochoka pamalopa ndikukalowa m'nyumba kuwasiya awiriwa akambirane.

Charles anamufotokozera chilichonse nzakeyo m'mene zinakhalira.
"Owo moti basi ntchito akuchotsani apapa ndiye mutanino? ".
" Ineyo kunena zooona sindikudziwa choti nkuchita ndi m'mene zakhaliramu". Ali choncho phone ya Charles inayitana.

Charles anapisa mu thumba la trouser lake ndikutulutsamo phone yo, atayang'ana yemwe anali kuyimbayo anali mayake.
"Charles". Anafikira kuyankhula mayi ake a Charles, ndi m'mene anali kumvekeramo zimachita kuonetseratu kuti anali kudandaula
" Amayi mawu anu sakumveka bwino chachitika ndi chani? ". Anafunsa Charles.
"Paja ndinakuuza kuti ndinangongola ndalama ku gulu yoti ndimulipilire m'chemwali wakoyi mayeso eti".
" Eya ndakumbukira munandiuzapo".
"Eya nkhani yake ndi imeneyo ndiye ineee ndalamayo mpaka pano sindinayibwenzebe moti agulu anabwera anyamukanso Pompano, akuti ngati sindibwenza ndalamayo abwera adzangosasula nyumbayi chifukwa m'nyumbamu mulibe choti angatengemo ndiye ineyo ndalamayo ndilibe ndi chifukwa ndikukuuza iweyo".
" Eeee koma zinthu zake, nanenso ntchito andichotsa lero moti ndalamanso ndilibe koma mwina ngati ndingasakesake ndiye kuti...

Asanamalize kuyankhula phone ija inaduka.
"Eee koma zinthu zake".
" Waonatu zomwe ndinkakuuza zija mayako nawo ndiawa akufunanso chithandizo apapa ukungoyenera kusakasakanso ntchito chifukwa ngakhale ineyo kandalama komwe ndimapezaka sikangatikwanire tonse.

Masiku anayi anali atadutsa, Charles anali atakhala pakhonde, apa ndikuti Brenda anali akuchapa zovala. Awiriwa anali kukamba nkhani zawo.

Felix anafika pamalopa.
"man kwapezeka ganyo tu uku ". Anayankhula Felix.
" Ganyo wanji ameneyo? ".
" Yotuta mchenga pa mtundapo pomwe pakumangidwa nyumba po".
"Aaaaa ndiye ndipite ndikayilowetu mwina nkupezako inayake ".
" Eya tiyeko limodzi nane ndidzibwelera ndinangobwera kudzakudziwitsa".

"Brenda tikupezatu".
" Chabwino ". Anayankha Brenda.

Charles ndi Felix anachoka pakhomopa ndikupita komwe kunali kututidwa mchengako.

Brenda atamaliza kuchapa zovala zija anakakhala pa khonde ndikumvera nyimbo mu phone . Ali choncho kunatulukira Emily.

" Ndi Emily kodi ndakulandira". Anayankhula Brenda.
"Zikomo, ndamuona mamuna wako akututa mchenga pa mtundapo kodi ndiye yoyendetsa tax ija anasiya? koma ndiye ku banja kuno ukuvutikatu".
" Ndikuvutika wakuuza ndani kuti ndikuvutika? ". Anafunsa Brenda.
" Nanga mamuna wako ngati wachoka koyendetsa galimoto ndikuyamba yotutira mchenga sikuvutika?.komanso m'mene wakutengera muja mukungokhalabe nka nyumba kothinana chonchi anthu atatu, mukuchita kukanika kupeza nyumba yanu yanu yoti ndikumakhala panokha apa ndinkakuuzatu koma ine apa ndiye mudzingokhalira kuvutikaku".

Ikupitilira........

BEHIND THE MIRRORCHAPTER 3Tinasiyilaaa pamene a police amafuna kumumanga Charles ndipo Brenda anabwera nkudzaima kutsogo...
14/08/2024

BEHIND THE MIRROR

CHAPTER 3

Tinasiyilaaa pamene a police amafuna kumumanga Charles ndipo Brenda anabwera nkudzaima kutsogolo kwa Charles..

"Iwe Brenda ndiye ukuona ngati ukupanga chani?, tachokapo pamenepo". Anayankhula molusa bambo a Brenda.
" Madala ndakamba kale kuti ngati mukufuna kuti Charles amangidwe, timangidwira limodzi ndi ineyo chifukwa sindingalore kuti akagone kundende komanso mukamumangitsa mukuona ngati andisamala ineyo ndi ndani?. Charles sikuti akufuna athawe ayi komano ndalama ndi yomwe ikuvuta kuti ayipeze moti ikapezeka abwera adzapereke komanso ngakhale kumumangako ndalamayo ayipeza bwanji? ".Anayankhula Brenda mopanda mantha ndipo bambo ake sanayankhe kalikonse.
" Bambo, ndimaona ngati zomwe akunena mwana wanuzi ndizoona mukanakhala kaye nkukambirana ". Anayankhula wa police wina.
" Chabwino basi musiyeni, komano asaone ngati ndalama yangayo ndamusiyila ndikaona kuti sakubwezabe mubweranso mudzamutenge ameneyu ; ukumva iwe wapulumuka chifukwa cha awawa sikuti ndakusiya ayi.. inu basi tiyeni tidzipita". Anayankhula bambo a Brenda ndikuchokapo pamalopa ndi apolisi aja.

Pamene anali kunyamuka naye Emily, nzake wa Brenda anali kufika pamalopa naye Charles anangopita ndikukalowa m'nyumba, nzake Felix anamutsatiranso m'nyumba m'momo.Emily anayesela kuwapatsa moni bambo a Brenda anangomuyang'ana sanamuyankhe kalikonse.

"Brenda chikuchitika ndi chani?, nanga bambo ako ndi a police wo amadzatani kunoko? bwanji nkhope yako ikuoneka chonchi? tandiuze nzanga". Anafikira kumufunsa mafunso omwe sakanatha kuyankha nthawi imodzi Brenda.
" Wafikiratu kufunsa mafunso ochuluka, tiye tikhale kaye pansi pakhondepa".

Awiriwa anapita ndikukakhaladi pakhonde.

"Mwaonatu man zomwe zakuchitikiranizitu apapa ndiye bola mukanangothawa basi". Anayankhula Felix.
" Umati ndithawe ndipite kuti? ndiye mkazi wanga nkanamusiyira ndani? komanso nkathawe mimba zoona? ndiponso ndimaona ngati nkhani imeneyi ingotha m'mutu mwanga mukuyenda kale zambiri apapa".
"Chabwino koma...
" Koma chaninso ndati sindikufuna kumvaso nkhani imeneyo ndisiye ndipume chonde".

"Ndiye tafokoza wati zakhala bwanji kuti bambo ako abwere ndi apolice kunoko? ". Anafunsanso Emily.
" Nkhani yake ndiyokuti, monga ukudziwira ndili ndi mimba ndiye bambo anga atauzidwa anamuyitanitsa Charles ndipo anamuuza kuti awabwezere ndalama yomwe anandilipilira fees ndiye chifukwa choti Charles ndalamayo analibe anawauza kuti amupatse mpata asakesake kaye komano ndalamayo sanayipezebe mpaka pano. Apapa ndipamene anabwera ndi a police kuti adzamumange ".
" Owoo ndamvetsetsa, ineyo ndimadabwa kuti sukubwera ku school moti ndinapita kwanu kuti ndidzafunse chifukwa chake komano sindinakupeze ndi pamene mayako anandiuza kuti uli kuno kubanja komano zoti uli ndi mimba ndinali ndikudziwa koma zoti uli ku banja sindinadziwe".
"Eya m'mene zinalilimo sindikanapeza mpata okudziwitsa komano ndizokuti bambo anga anandithamangitsa tsiku lomwelo".
" Chabwino ndakumvetsa, ndiye ine ndidzibwelera kunyumba ndidzabweranso tsiku lina".
"Chabwino tiyeko ndikusiye apo".

Brenda ndi nzake Emily anachoka pamalopa ndikumaperekezana akukamba nkhani zawo mpaka anakafika pa malo ena.
" Komano Brenda unaganiza bwanji iweyo ".
" Kuganiza bwanji kwa chani? ".
" Monga iweyo sukudziwa chomwe ndikutanthauza".
"Ndiye ineyo ndingadziwe bwanji chomwe ukutanthauza munthu wangoyambira pakati nkhani yakoyo".
" Ndikutanthauza kumutchula Charles kuti ndi mwini wake wa mimba, ukanamvera zomwe ndimakuuza zija sibwenzi zinthu zilitu chonchi, taona apa ukuti mamuna wako akuchita kukanika kubwenza ndalama ya fees kwa bambo ako , apanso akuti akukwatira koma mukukhalabe mu kanyumba kamodzi ndi nzake wa Charles kusonyeza kuti sangakusamale bola ukanangomupaka mamuna wa ndalama osati a Charles wa".
"Basi ndi zomwe umafuna kundiuza? ".
" Kusonyeza zomwe ndakuuzazi ndizosakwanira?, Brenda ineyotu ndi nzako yekhayo ndipo ndikungokufunira zabwino chabe ndi chifukwa ndimakuunikira".
"Owo zikomo chifukwa chondiunikira uyenda bwino".
" Koma Brenda".

Brenda anangochokapo pamalopo ndikumabwelera kwawo nkumusiya nzakeyo pomwepo.
"Akunyanyala chifukwa ndikumuunikira zabwino, anthu opanda pabwino, akanamupaka mamuna wa ndalama uja sibwenzi zinthu zili chonchi". Anali kudziyankhulira yekha naye anabwelera kwawo.

Bambo a Brenda anafika kwawo akuoneka olusa, anawapeza akazi awo akuchapa zovala; anangowadutsa akazi awowo ndikukalowa m'nyumba. Nawo akazi awo anawatsatira m'nyumba m'momo.

" Mukuoneka olusatu, mwayenda bwanji kumeneko? ".
" Aaaaa mwana wako uja kutereku anapangitsa kuti mamuna wakeyo asamangidwe akuti akusakasakabe ndalamayo ndiyee ndamuuza kuti ngati sabweretsa ndalamayo ndipitanso akakumangidwa basi chifukwa ine ndimadana ndi zopusa sindipereke feees iyeyo nkusankha kutenga mimba".

Mayi a Brenda anachoka pomwe analipo ndikukakhala pa mpando omwe anakhalapo amuna awowo, anawagwira pa phewa.
"Amuna anga, mukudziwa chani ineyo sikuti ndikuyikira kumbuyo zomwe anapanga Brenda zo komano ndimaona ngati bwenzi mamunayo mwangomusiya kuti asabwezenso ndalamayo chifukwa ngakhale m'mene akuonekera muja ndalama yochuluka choncho ".
" Sangakwanitse choncho ndiye kuti chani?, kodi m'chifukwa chani nthawi zonse umamuyikira kumbuyo mwana ameneyu?, chabwino ngati salipira ndiye kuti ndikumumangitsa basi".
"Sikuti ndikumuyikira kumbuyo komano ndikungoyankhula m'mene zimayenera kukhalira komanso mukamumangitsa mamuna wakeyu ndiye kuti mwana wathuyo akhala pamavuto komanso palibe chomwe chingasinthe ; mukumbukire Brenda ndi mwana wathu yekhayo yemwe tili naye".
" Chabwino ndamva ndikuona ngati ndingozisiyadi".

Ikupitilira.....

BEHIND THE MIRRORCHAPTER 2"chabwino sindikufuna zambiri ayi, poti fees yomwe amalipira iyeyu ukuiziwa, ndipo wafuna ndi ...
13/08/2024

BEHIND THE MIRROR

CHAPTER 2

"chabwino sindikufuna zambiri ayi, poti fees yomwe amalipira iyeyu ukuiziwa, ndipo wafuna ndi iwe kuti asiye school osati inenso, ndiyeno ndikufuna fees yanga yomwe ndalipira ku school term ino bas k350,000, Pompano".

Charles anangoti kakasi, kusowa choyankha apa ngakhale ndalama yoti akagule chakudya analibe, anali ndi maganizo ndalama yonseyi ndichoka nawo kuti......

"komano sir mwaulemu wake bwanji mutandipasako mpata pang'ono kuti ndikhale ndikusaka ndalama imeneyo".
"ndikuti ndikuifuna Pompano osati za mawazo."
"ndalama ndi yambiri sindingaipeze lero ndi lero, ndamukonda mwana wanu sindingamusiye chifukwa mwandilamula zoti ndibweze ndalama ya fees ayi".
"ukuziwa Usamandilakhule zachamba apa wamva, ndiye iwe Brenda mwamuna wako akudikira kuti alipire ndalama apa iwe pita mnyumba uzikapakira zinthu zako chilichonse chomwe chili chako uchose mnyumba muno chifukwa ukachoka suzabweranso".
"koma dad".
"Ukundiziwa sindikufuna kubwereza zinthu kawiri,panga zomwe ndakuuza Pompano".
"koma amuna anga, musapere chigamulo mwachangu musaiwale kulinso mawa".
"ndiye kuti zikukusangalasani zomwe wachita iyeyu eti, kapena munapangana, ndizomwe mumapanga mukasala pakhomo pano".
"ayinso chabwino m***a kupereka chigamulo chomwe mukufuna basi simundimvanso ndikuikira mulomo nkhani imeneyi".
"Brenda panga zomwe ndakuuza ndipo mnyamata iwe utha kupanga zomwe ndakuuza, ukachedwa police ibwera kuzakutenga ndipo ndili serious".

Brenda misonzi inayamba kugwa kwinaku akupita ku chipinda kwake kukapakira zinthu zake.

"Mr muli apa ndilore ndisake ndalama, ngakhale mundiitanire police sizipangisa kuti ndalama ikuluke pomwe ine ndilibe apo pokha ndiye ndikunamizani".
"ukupanga zibwana ndi ine eti?, ukuyenda ngati ndikuseka kapena?,".
"ndikuziwa kuti nkhani ndiya serious, ndipo apa ndili serious, chonde ndimveseseni mwina Ndikanakhala kuti ndikukana zoti mimba si yanga bwenzi mukukamba za police apa ndavomera komanso ndalama yanu ndikupasani".

Brenda anapamaliza kupakira zinthu zake anabwelera pa sitroom paja.

"well mnyamata, Brenda lero sakugona Kuno umunyamula kupita naye kwanu, ndikupasa week imodzi, ndiye ndikuuze palibe komwe ungathawire".
"palibe komwe ndingapite, Zikomo kwambiri pondimvesa".

Charles ndi Brenda Anatengana kupita kwawo.

Kanyumba komwe amakhala Charles ndi mzake Micheal kanali kakang'ono kopanda chipinda nkomwe.

Micheal anamutengera, mzake Charles pambali.

"Charles apa Brenda yemwe ndi nkadzi wako wabwera mnyumba muno koma Pali vuto limodzi".
"vuto lanji?,".
"Charles ukunena chilungamo sukuziwa vuto lake, tilipo anthu atatu sopano, malo ogona zikhala bwanji?".
"apa zinthu zavuta kale komanso ndilibe ndalama yoti ndingathe kukhala pa dekha please ndimvese, zikayamba kuyenda ndizasamuka".

Micheal anapumila mmwamba....

"chabwino ndakumvani pamenepo".

Charles analowa mnyumba kumuitanira Brenda panja...

"Charles ndiye makhalidwe ake tizikhala motani nyumba kakang'ono ngati kameneka".
"well, poti zavuta tizikhala movuta momwemo and ndikupepha kuti chomwe uzipase ulemu wekha ukuona kanyumba kakang'ono komanso tili anyamata awiri".
"Osadandaula Charles, ndikuziwa zoti muli ananyamata awiri, sindipanga zibwana zilizonse".
"ndimamukonda kwambiri Brenda".
"inenso Charles ndipo ndalimba mtima kuti tivutikire limodzi basi pa ulendo umenewu".

Awiriwa anayang'anizana, kupasana kiss...
____

Emily anadabwa mzake Brenda sakumuona komanso ku school sakupita.

Iye anaganiza zoti apite kwawo akamuone, mmaganizo mwake amati mwina akudwala.

Atafika anagogoda pakhomo.. Ndipo anatuluka anali mayi ake a Brenda apa Bambo ake anali ali ku ntchito.

"Emily Ulipo koma ndiye ungaziwe kusowa".
"ndilipo amayi kungoti mukuziwa kale ndiza school zaku zija basitu mpata ukusowa".
"paja ana a school ndinaiwala lowantu nanga".
"mmmmhhh mwina nditha kulowa amene ndikufuna palibe".
"unena Brenda?".
"eya kudabwa ku school sakubwera".
"kodi sanakuuze zomwe zachitika".
"ayi sindikuziwa kalikonse".
"takhala apa ndikuuze".

Emily anakhala pampando omwe unali pakhonde.

"mzako Brenda, ali ndi mimba moti ndikunena pano Bambo ake anam***amangisa ali ku banja kwawo kwa mwamuna wake.
"mimba Brenda?, sozakhala bwino ngakhale pang'ono, Zikomo kwambiri amayi pondiziwisa ndimusaka komwe ali ndikamuone".
"Zikomo".
"basi ndinyamuke".
"uyende bwino, mwana wanga".

Komatu zonsezi zoti Brenda Ali ndi mimba Emily ankaziwa ndithu, koma zoti ali kwa mwamuna wake samaziwa kalikonse, anakoza tsiku loti apite akamuone.
___
Patatha sabata ziwiri pomwe Charles anauzidwa kuti abweze ndalama zikwana k350,000, kwa Bambo ake a Brenda.

"mwamuna wake a Brenda sakufuna kubweresa ndalama zanga akufuna ndigwirise ntchito mphavu sopano kapena akuyesa ngati ndaiwala".
"dekhan amuna anga munthu uja zikuonesa ngati alibe ndalama akusakabe".
"ndimupitira kwawo komweko".
"mukuziwa komwe amakhala?".
"eya, ndinamufufuza kale".

Mmawa wake Cha mma 10 o'clock Mmawa Bambo a Brenda anakatenga police ulendo wa kwa Charles.

"Charles tuluka apa chanu". Bambo a Brenda Anakuwa akumenya Chiseko.

Anakuluka anali Brenda koyamba Kenako Charles.

"police nyamata wake ndi ameneyu mtengeni".

Kuti azimumanga Brenda anathamanga kuima kusogolo kwa Charles.

"madala ngati mukufuna kupanga Charles mumange limozi ndi ineyo.......

Ikupitilira.........

Address

Blantyre

Telephone

+27769972692

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Christina Stories posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category