01/06/2026
MLEMBI WAMKULU MU UNDUNA WA ZA MPHAMVU ANAYENDERA NDIKULIMBIKITSA OGWIRA NTCHITO KU PULOJEKITI YA ASCENT
Lero, Mlembi Wamkulu mu Unduna wa za Mphamvu, a Elvis Thodi, anayendera ofesi ya pulojekiti ya ASCENT pofuna kuwunika momwe ntchito zikuyendera, kulimbikitsa kufunika kogwira ntchito motsatira nthawi, komanso kumva mavuto omwe ogwira ntchito akukumana nawo. Ulendowu ukuwonetsa kudzipereka kwa Unduna pakuwonetsetsa kuti ASCENT ikupereka zotsatira zenizeni kwa a Malawi.
ASCENT (Accelerating Sustainable and Clean Energy Access Transformation) ndi pulojekiti yothandizidwa ndi Banki ya Dziko Lonse (World Bank) yomwe ikugwiridwa ntchito limodzi ndi Unduna wa za Mphamvu ndi ESCOM. Cholinga chake ndi kukulitsa mwayi wopeza magetsi komanso kulimbikitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zophikira zotetezeka zosawononga chilengedwe kuti zitukule moyo wa anthu komanso chuma. A Thodi ,analimbikitsa mgwirizano wolimba pakati pa onse okhudzidwa kuti ntchito ziziyenda bwino.
Mu mau ake, Mlembiyu anatsindika kufunika kwa kuzipeleka kogwira ntchito mwaukadaulo, komanso kugwiritsa ntchito bwino chuma cha pulojekiti, kuti ASCENT ikwaniritse cholinga chake chokulitsa mwayi wopeza magetsi m’Malawi
Ngwee Ngwee Ngwee Fund