28/08/2026
NRB MOGWILIZANA NDI ACB AWONJEZERA NDONDOMEKO ZOLIMBANA NDI KATANGALE
Bungwe la National registration Bureau NRB lakonza ndondomeko zowonjezera polimbana ndi katangale.
Bungweli lakonza ndondomekozi ku nkumano womwe linachita ku Mponera Mboma la Dowa, pamodzi ndi a bungwe la Anti Corruption Bureau ACB.
Poyankhula ku msonkhanowu mkulu wa bungwe la NRB a Patrick Machika anathokoza bungwe la ACB pothandizila kuti NRB lichepetse chiwophyezo cha katangale pogwila ntchito yake.Iwo anatsimikizila kuti Bungweli lichita zonse zotheka kulimbana ndi katangale, ndi kuthana ndi omwe akuchita ntchitidwewu.
Nkulu wa za chilungamo mu unduna wa za chitetezo mayi Mary Phombeya anayamikila bungwe la NRB pokonza nkumanowu kuti uthandize kuwunika ntchito za bungweli ndi kuthana ndi katangale.