DPP Central Region Updates

DPP Central Region Updates Promoting Democratic Progressive Party's events and functions being implemented in the central region
(1)

08/06/2024

NTCHITO ZOPITITSA CHIPANI PA PATSOGOLO ZIKANALI MKATI

Bwanankubwa (DG) wa Lilongwe urban, bambo M***a Saidi Kunkhokwe ali ku Chigwiri Ward komwe akupereka uthenga wabwino wachiyembekezo kwa ma membala achipani cha DPP.

Bambo Saidi ati m'nthawi imene DPP inali m'boma kuyambila nthawi ya malemu Prof. Bingu wa Mutharika (nzimu wao upitirire kuunsa mu mtendere) komanso mu nthawi ya President Prof. APM chilichonse chinali m'chimake.

"Lero tikuchitila umboni kuti DPP motsogozedwa ndi President wathu Prof. APM inakwanitsa kupereka utsogoleri wabwino. Munthawi ya DPP panalibe m'malawi amene anatisiya chifukwa cha njala komanso DPP inkaonetsetsa kuti chitetezo chikhale m'chimake" atero a DG, Hon Saidi

Ena mwa anthu amene anali nawo pa msonkhanowu ndi monga Mr Andrew Kowedza, Mr Namakhwa komanso akulu akulu ena amu committee ya Lilongwe Urban District. Masapota achipani cha DPP ati okondwera ndi momwe a DG akugwirila ntchito yotukula chipani mu Lilongwe District.

DPP woyeee!!!!!!
Prof. APM woyeee!!!!!!
Hon AG woyeee!!!!!!
Hon RG woyeee!!!!!!
Hon DG woyeee!!!!!!

02/06/2024

ANTHU AKUFUNITSITSA CHIPANI CHA DPP KUTI CHILOWE M'BOMA-- SNR DG Hon Saidi Kunkhokwe

A Snr DG Hon M***a Saidi Kunkhokwe atsindika kuti amalawi atopa ndi ulamuliro umene ulipowu poti walephera kukwaniritsa zomwe unalonjeza. A Kunkhokwe ayankhula izi lero kwa Mtsiriza komwe anapita ndi komiti yawo kukakumana ndi adindo achipani aku constituency ya Mtsiriza komanso Mtandire.

Constituency ya Mtsiriza motsogozedwa ndi agavanala bambo Vincent M'nonolo yati sizochitanso kufunsa kapena kukaikila,DPP yanyamuka ndipo masapota nawo pa ground akonzeka kumema anthu ochuluka kuti alimbikitsane wina ndi nzake zokavotera chipani cha DPP.

A Snr DG, Hon Saidi M***a ati iwo monga a District gavanala a Lilongwe Urban akonzeka kuponda paliponse mu Lilongwe Urban komanso kuthandizila ma DGs ena amadera ena kupititsa patsogolo ntchito za chipani. A Kunkhokwe dzulo anali ku Kawale Masintha ward komwe amagwira ntchito zinaso za chipani ndipo lero anaona kuti ndikofunika kuti akacheze ndi anthu akwa Mtsiriza komanso Mtandire. Ndipo ati sayiira pomwepa ntchitoyi.

DPP 2025 Boma
Prof. APM woyeeeee
Hon AG VP woyeeee
Hon RG woyeeeee
Snr DG Woyeeeee
LL Urban Woyeeee

KULIMBIKITSA  CHIPANI KU CONSTITUENCY KOMANSO KU AREA, MASINTHA CONSTITUENCYA Senior District Governor a Lilongwe Urban,...
02/06/2024

KULIMBIKITSA CHIPANI KU CONSTITUENCY KOMANSO KU AREA, MASINTHA CONSTITUENCY

A Senior District Governor a Lilongwe Urban, bambo M***a Saidi kunkhokwe akupitiriza kudzutsa ma area komanso kulimbikitsa ntchito za chipani ku ma area a chipani cha DPP. A kunkhokwe dzulo anayendera constituency ya Masintha yomwe agavanala ake ndi bambo Schinga.

A senior DG pa msonkhanowu analimbikitsa achinyamata, amai komanso a bambo kuti apitirize kugwira modzipereka ntchito za chipani cha DPP. Iwo ati pamene chinsakho chikubwera ndikofunika kuti ma membala achipani cha DPP akhale olimba.

A DG pamene ati masankho ali nkudza ndikofunika kuti tonse tikalembetse chiphaso pakuti nthawi yochotsa Tonse Alliance pa mpando yakwana ndipo zonsezi kuti tizikwaniritse tikalembetse chiphaso mwa unyinji. A DG anatinso chipani cha DPP ndi manthu wa chitukuko komanso mfundo ndipo chimalimbikitsa bata ndi mtendere.

"Tinaona msonkhano wa DPP ku mjamba (Blantyre) m'mene unalili ndipo tinauzidwa kuti ADADI President Prof. Arthur Peter Mutharika akubweranso kuno ku central region (Lilongwe) ife takonzeka kudzaposa unyinji wa anthu omwe unapita ku Mjamba." Anatero a Snr DG, Hon Saidi M***a Kunkhokwe

A Boniface Sichinga pamodzi ndi constituency yonse ati ndionyadila kaamba ka kubwera kwa Hon DG komanso committee yawo yonse ku Masintha constituency iwo zomwe ayankhula a Snr DG ziwapatsa mangolomera ndipo chipani chikudzapambana ndi mavoti migolomigolo.

DPP woyeeee
Lilongwe Urban District Woyeee

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when DPP Central Region Updates posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share