08/06/2026
M̲i̲t̲u̲n̲d̲u̲ ̲y̲a̲ ̲Z̲i̲p̲h̲a̲s̲o̲ ̲z̲o̲m̲w̲e̲ ̲M̲M̲R̲A̲ ̲i̲m̲a̲p̲e̲r̲e̲k̲a̲ ̲p̲a̲n̲s̲i̲ ̲p̲a̲ ̲l̲a̲m̲u̲l̲o̲ ̲l̲a̲ ̲M̲i̲g̲o̲d̲i̲ ̲n̲d̲i̲ ̲M̲i̲y̲a̲l̲a̲ ̲y̲a̲ ̲M̲t̲e̲n̲g̲o̲ ̲W̲a̲p̲a̲t̲a̲l̲i̲,̲ ̲l̲a̲ ̲2̲0̲2̲3̲ ̲(̲M̲i̲n̲e̲s̲ ̲a̲n̲d̲ ̲M̲i̲n̲e̲r̲a̲l̲s̲ ̲A̲c̲t̲,̲ ̲2̲0̲2̲3̲
𝟭. 𝗖𝗵𝗶𝗽𝗵𝗮𝘀𝗼 𝗖𝗵𝗼𝗳𝘂𝗳𝘂𝘇𝗮 𝗰𝗵𝗮 𝗮 𝗠𝗮𝗹𝗮𝘄𝗶 𝗼𝗴𝘄𝗶𝗿𝗮 𝗻𝘁𝗰𝗵𝗶𝘁𝗼 𝘇𝗮 𝗺𝗶𝗴𝗼𝗱𝗶 𝗶𝗻𝗴’𝗼𝗻𝗼𝗶𝗻𝗴’𝗼𝗻𝗼 (𝗡𝗼𝗻-𝗘𝘅𝗰𝗹𝘂𝘀𝗶𝘃𝗲 𝗣𝗿𝗼𝘀𝗽𝗲𝗰𝘁𝗶𝗻𝗴 𝗟𝗶𝗰𝗲𝗻𝗰𝗲)
📌Ndi cha nzika zaku Malawi kuti zifufuze m’zigawo zopitirira zitatu zolumikizana popanda kugwiritsa ntchito makina olemera.
📌 Ziphaso zingapo zitha kuperekedwa pa malo omwewo, kutanthauza kuti chiphasochi sichiletsa anthu ena kudzagwira ntchito pamalo pomwe pali kale chiphaso ngati chimenechi.
📌Chiphasochi chimaperekedwa kwa chaka chimodzi komanso chimapereka mwayi odzatengedwanso kwa chaka choonjezera chimodzi.
📌 Chiphasochi ndichokufufuzira pogwiritsa ntchito njira zosavuta monga makasu ndi mafosholo.
𝟮. 𝗖𝗵𝗶𝗽𝗵𝗮𝘀𝗼 𝗖𝗵𝗼𝘆𝗮𝗺𝗯𝗮 𝗸𝘂𝗳𝘂𝗳𝘂𝘇𝗮 (𝗥𝗲𝗰𝗼𝗻𝗻𝗮𝗶𝘀𝘀𝗮𝗻𝗰𝗲 𝗟𝗶𝗰𝗲𝗻𝗰𝗲)
📌Chimalola kufufuza malo a mulingo wama kilomita 100,000.
📌 Kuletsa kusokoneza pamwamba pa nthaka pokhapokha ngati wavomerezedwa.
📌 Njira zofufuza kuchokera ku kauniuni wam’malere kapena mulengalenga.
📌 Chiphasochi nachonso sichiletsa anthu ena kudzagwira ntchito zamigodi pomwe ichochi chaperekedwa.
𝟯. 𝗖𝗵𝗶𝗽𝗵𝗮𝘀𝗼 𝗖𝗵𝗼𝗳𝘂𝗳𝘂𝘇𝗮 𝗠𝘄𝗮𝘁𝘀𝗮𝘁𝗮𝗻𝗲𝘁𝘀𝗮𝘁𝗮𝗻𝗲 (𝗘𝘅𝗽𝗹𝗼𝗿𝗮𝘁𝗶𝗼𝗻 𝗟𝗶𝗰𝗲𝗻𝗰𝗲)
📌Chimapereka ufulu onse ofufuza mwatsatanetsatane miyala ya mtengo wapatali pa dera lomwe chaperekedwa, kuphatikiza mpaka kafukufuku owona kuthekera kozachita ntchito yamigodi pamalo.
📌Ziphaso za migodi yaing’ono zitha kuperekedwa m’malowa ngati wavomerezedwa.
📌 Chiphasochi chimaperekedwa kwa zaka zisanu, komanso pamakhala kuthekera kotenganso chiphasochi kwa zaka zina zitatu ndipo izi zikhonza kuchitika kawiri.
4. 𝗖𝗵𝗶𝗽𝗵𝗮𝘀𝗼 𝗖𝗵𝗼𝘀𝘂𝗻𝗴𝗮 𝗠𝗮𝗹𝗼 (𝗥𝗲𝘁𝗲𝗻𝘁𝗶𝗼𝗻 𝗟𝗶𝗰𝗲𝗻𝗰𝗲)
📌 Ndi cha omwe ali ndi chiphaso chovomerezeka chofufuza omwe apeza miyala ya mtengo wapatali koma sangayambepo kukumba miyalayi pazifukwa zosiyanasiyana.
📌 Chimakhala chovomerezeka kwa zaka zisanu, sichionjezeredwanso.
5. 𝗭𝗶𝗽𝗵𝗮𝘀𝗼 𝘇𝗮 𝗠𝗶𝗴𝗼𝗱𝗶 𝗬𝗼𝗸𝘂𝗹𝗶𝗿𝗮𝗸𝗼 𝗣𝗮𝗻𝗴’𝗼𝗻𝗼 𝗻𝗱𝗶 𝗬𝗮𝗶𝗸𝘂𝗹𝘂 (𝗠𝗲𝗱𝗶𝘂𝗺 𝗮𝗻𝗱 𝗟𝗮𝗿𝗴𝗲-𝗦𝗰𝗮𝗹𝗲 𝗠𝗶𝗻𝗶𝗻𝗴 𝗟𝗶𝗰𝗲𝗻𝗰𝗲𝘀)
📌 Zimapereka ufulu wokumba ndikutulutsa miyala ya mtengo wapatali.
📌 Pali milingo yokhanzikitsidwa ndi malamulo yomwe imanena ngati chiphaso cha mgodi waukulu chili choyenera kuperekedwa, monga ndalama zolowetsedwa pomanga mgodi zokwanira kapena kupyola 250 million dollars yaku America, kulemba ntchito anthu opyola 1000, ndi katulutsidwe ka miyala yopyola 5 million tonnes kuphatikiza miyala yotsala mgodi ukakhala otsegula, 500,000 tonnes mgodi ukakhala wapansi pa nthaka, ndi 1 million cubic meters mgodi ukakhala ofukula michenga .
📌Chiphasochi chimaperekedwa kwa zaka zosapyola 25 ndipo chimatha kuzaperekedwanso kwa zaka 15 ngati kuli koyenera kutelo.
6. 𝗖𝗵𝗶𝗽𝗵𝗮𝘀𝗼 𝗰𝗵𝗮 𝗠𝗶𝗴𝗼𝗱𝗶 𝗬𝗮𝗶𝗻𝗴’𝗼𝗻𝗼 (𝗦𝗺𝗮𝗹𝗹-𝗦𝗰𝗮𝗹𝗲 𝗠𝗶𝗻𝗶𝗻𝗴 𝗟𝗶𝗰𝗲𝗻𝗰𝗲)
📌 Chimalola nzika zaku Malawi kukumba Miyala ya Mtengo wapatali m’malo osapitirira mahekitala awiri komanso osachepera hekitala imodzi.
📌 Chimaperekedwa kwa zaka ziwiri ndipo pamakhala kuthekera kochiperekanso kwa zaka zina ziwiri malingana ndikufunikira kwake.
📌Sichimalora kugwirisa ntchito makina olemera.
7. 𝗖𝗵𝗶𝗽𝗵𝗮𝘀𝗼 𝗰𝗵𝗼𝗴𝘂𝗹𝗮 𝗻𝗱𝗶𝗸𝘂𝗴𝘂𝗹𝗶𝘁𝘀𝗮 𝗺𝗶𝘆𝗮𝗹𝗮 𝘆𝗮 𝗺𝘁𝗲𝗻𝗴𝗼 𝘄𝗮𝗽𝗮𝘁𝗮𝗹𝗶 (𝗥𝗲𝘀𝗲𝗿𝘃𝗲𝗱 𝗠𝗶𝗻𝗲𝗿𝗮𝗹𝘀 𝗟𝗶𝗰𝗲𝗻𝗰𝗲)
📌 Ndi chiphaso cha malonda chogula ndi kugulitsa mitundu yololezedwa ya miyala ya mtengo wapatali.
📌Chiphasochi chimaperekedwa kwa chaka chimodzi ndipo chili ndikuthekera koonjezera nthawiyi kwa chaka chinanso.
𝗭𝗶𝘄𝗮𝗻𝗶 𝗶𝘇𝗶:
📍kukumba Miyala ya Mtengo Wapatali Opanda Chiphaso ndi Mlandu.