12/08/2026
First Capital Bank yapereka zida zogwiritsa ntchito pa nkhani ya zaukhondo komanso za ndalama yokwana K6 miliyoni ku khonsolo ya boma la Mchinji, zomwe zithandizire, kukwaniritsa Lamulo la Pulezidenti Nambala 2 lokhudza ukhondo, lomwe linakhadzikitsidwa ndi Purezidenti Professor Arthur Mutharika.
Zidazi zikuphatikizapo ma wilibara 20, mafosholo 19, ndi nsapato zozitetezera 20.
Polankhula pamwambo woperekera zidazi, Bwanankubwa wa Boma m’boma la Mchinji a Reinghard Chavula, anati khonsoloyi yakhala ikukumana ndi vuto la kusowa kwa zida ndi zipangizo zofunika pa nkhani ya ukhondo m’malo mumene mumapezeka anthu ambiri.
“Monga khonsolo, tinali ndi kusowekera pankhani ya zida ndi zipangizo zokonzera malo kuti akhale aukhondo mu malo opezeka anthu ambiri. Thandizoli labwera pa nthawi yoyenera ndipo lithandiza kwambiri kuti tikwaniritse Lamulo la Pulezidenti lokhudza ukhondo ndi usafi,” adatero Chavula.
Mkulu woyang'anira thambi za First Capital Bank m’chigawo cha chapakati a Zizwa Gondwe, anati bankiyo yasankha kuthandiza Mchinji pambuyo poti khonsoloyi inapempha thandizo li.
Thandizoli lilimbikitsa mphamvu za khonsoloyi pa ntchito za ukhondo mmisika, malo okwelera ma basi ndi malo ena opezeka anthu ambiri, pamene ikupititsa patsogolo ntchito zokwaniritsa lamulo la Pulezidenti lokhudza ukhondo.