Salima District Council

Salima District Council Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Salima District Council, Government Organization, Salima.

22/08/2026
Mneneri wa bungwe lobwereketsa ngongole kwa ana a msukulu zaukachenjede la Higher Education Students' Loans and Grants B...
21/08/2026

Mneneri wa bungwe lobwereketsa ngongole kwa ana a msukulu zaukachenjede la Higher Education Students' Loans and Grants Board (HESLGB) Mercy Chijere wati ntchito yosankha amene ali oyenera kutenga ngongoleyi yayenda bwino pomwe chiwerengero chakwera ndi 23.9%.

Iye wayankhula izi lachinayi pamkumano wa atolankhani omwe bungweli linaitanitsa.

Chijere wati mwa ana 46,3860 omwe adalembera ngongoleyi, ana 33, 258 ndiomwe asankhidwa.

Mwa anthu 33, 258 omwe asankhidwa, 27894 ndi anyamata ndipo nambalayi ikuimila 62.5%
Ndipo 17, 386 ndi atsikana kuimila 37.5%.

Chijere wati amene sanakhutire ndizotsatirazi ali ndiufulu opereka madandaulo motsata ndondomeko zoyenera.

Mkulu woyendetsa zintchito wa  bungwe la Solidaridad Moses Ching'ombe walimbikitsa alimi athonje kupanga manyowa a Bioch...
15/08/2026

Mkulu woyendetsa zintchito wa bungwe la Solidaridad Moses Ching'ombe walimbikitsa alimi athonje kupanga manyowa a Biochar kuchokera ku michakala ya thonje kusiyana ndikuotcha mitengo yotsalira akakolola.

Iye wayankhula izi lachinasanu pamene alimiwa amaphunzitsana kapangidwe ka Biochar ku S5 pansi pa pulojekiti ya Pathways to Prosperity Cotton mboma la Salima.

Mmawu ake Ching'ombe wati kupanga Biochar ndinjira imodzi yochepetsera mpweya woyipa mlengalenga, amasunga chinyezi komanso kuthana ndimatenda a mbozi mmunda.

Iye watiso izi zikutsatiraso zimene boma likufuna kuti anthu azipanga feteleza wa mbeya kuchokera ku feleteleza wamakono ndizipangizo zina za lokolo zomwe cholinga chake ndikubwezeretsa chonde kutsatira kuguga kwa nthaka.

Wapampando wa gulu la Mapesi, Alinafe Chadewa wati Biochar ndiwabwino kwa alimi ochepekedwa ponena kuti feteleza wamakono ndiokwera mtengo.

Mlembi wa gulu la Mapesi Beatrice Chisi walimbikitsa amayi kupezeka nawo mmagulu osiyanasiyana opindulitsa kusiyana ndikumangokhala.

Kupatula kuphunzitsa alimi Solidaridad ili pamngwirizano ndi nthambi zakafukufuku za Chitala, Bvumbwe, Chitedze komanso sukulu ya ukachenjede ya LUANAR.

Papita zaka ziwiri tsopano alimiwa akupanga manyowa a Biochar yemwe amathira mminda mwawo komanso kugulitsa kuti azipeza ndalama.

Mlangizi wachitikuko wa Khonsolo ya Salima Elina Lukas walimbikitsa ma membala a CDC kutsatira ndondomeko zoyenera poyen...
15/08/2026

Mlangizi wachitikuko wa Khonsolo ya Salima Elina Lukas walimbikitsa ma membala a CDC kutsatira ndondomeko zoyenera poyendetsa thumba la ndalama zokwana K5 billion za Constituency Development Fund (CDF).

Lukas wayankhula izi lachinayi atamaliza kuchititsa maphunziro a mamembala a ADC kuchigawo chapakati chakumadzulo kwa boma la Salima.

Iye wati ndikofunika kuti mamembalawa adziwe ndikumvetsetsa udindo wawo pa thumba la CDF komanso kukwaniritsa pokhazikitsa zitukuko za CDF.

Mwa zina, Lukas wati adindowa akuyenera kuonetsetsa kuti ndalama zagwira ntchito yoyenera komanso kuneneza omwe akuchita mkhalidwe lokayikitsa kwa akukuakulu achitetezo.

Lukas walimbikitsaso adindowa kuti asankhe zitukuko zofunikira kwambiri malingana ndindalama zomwe zilipo kuchokera ku thumba la CDF.

Maphunzirowa achitika mzigawo zonse zaboma la Salima

KUYENDERA NTCHITO ZOBWEZERETSA CHILENGEDWE KU LINTHIPE CATCHMENT AREAGulu la National Technical Supervision Team layende...
14/08/2026

KUYENDERA NTCHITO ZOBWEZERETSA CHILENGEDWE KU LINTHIPE CATCHMENT AREA

Gulu la National Technical Supervision Team layendera kwa Chagunda ndi kwa Gwirize ku Linthipe kuti liwone momwe CS-EPWP Phase 1 ya 2026 ikuyendera.

Anthu oposa 358 kuchokera kwa achagunda ndiomwe akupindula ndi ntchito zobwezeretsa chilengedwe popanga ma swale, akalozera, manyowa, kubzala mitengo, senjere ndi bango m’mbali mwa mitsinje, komanso kusamalira nkhalango.

Kwa Gwirize, anthu abzalapo senjere ndi bango m’mbali mwa mtsinje kwa makilomita 21 kuyambira chaka chatha.

Peter, membala wa gulu la Gwirize, wati ntchitoyi yathandiza anthu kuthana ndi njala komanso kusintha mmene amasamalirira chilengedwe.

Henry Hunga, Cluster Coordinator, wayamikira anthu chifukwa cha ntchito yabwino yomwe akugwira ndipo walimbikitsa anthuwa kuti asasiye ngakhale pulogalamuyi itatha.

11/08/2026

Nduna yowona za Mphamvu Jean Mathanga yati Boma likuyesetsa kuthana ndi vuto la magetsi pobweretsa njira zosiyana siyana zopangira magetsi.

Ndunayi yafotokoza izi pomwe yakhazikitsa magetsi ochoka ku dzuwa m'boma la Salima.

Magetsi okwana 10 Megawats ndi omwe akhazikitsidwa ndipo kutsogoloku awonjezeredwa kufika pa 50 Megawats.

Khonsolo ya Boma la Salima ikupereka mauthenga a momwe magulu a achinyamata ndi amayi angatengere ngongole mu thumba la ...
07/08/2026

Khonsolo ya Boma la Salima ikupereka mauthenga a momwe magulu a achinyamata ndi amayi angatengere ngongole mu thumba la Constituency Development Fund (CDF).

Ngongolezi ziziperekedwa kudzera ku bungwe lobwereketsa ndalama la Malawi Enterprise Development Fund (MEDEF).

Mlangizi owona zakusasiyana pakati pa amayi ndi abambo, anyamata ndi atsikana mu khonsoloyi, Friness Samaliya wati omwe akuyenera kutenga ngongolezi ndi achinyamata a zaka 18 mpaka 35, komanso amayi a zaka 35 mpaka 75.

Iye wati onsewa akuyenera kukhala ndichiphaso chaunzika komanso m'magulu a anthu 5 mpaka 10.

Samaliya wati ngongolezi ziperekedwa kwa amayi komanso achinyamata chifukwa ndiomwe nthawi zambiri amakhala ochepekedwa pankhani yazachuma.

Mlangiziyu wati ali ndichikhulupiliro kuti magulu ambiri alembetsa kuti ayese nawo mwayi otenga ngongole.yi.

Mlangizi oyang'anira achinyamata m'bomali Sharon Chilomo walimbikitsa amayi komanso achinyamata kupanga magulu odalilika posankha anthu omwe sadzavuta kubweza ngongoleyi.

Wapampando wa achinyamata kudera la mfumu yaikulu Ndindi Yolamu Khumbila Phiri wayamikira mkumanowu ponena kuti waatsekula maso zomwe zithandizire kutsata ndondomeko zoyenera pofuna kutenga ngongoleyi.

Boma kudzera ku MEDEF likupereka ngongolezi kuti amayi komanso achinyamata akhale odzidalira kumbali yazachuma popanga ma bizinezi osiyanasiyana.

Address

Salima

Opening Hours

Monday 07:30 - 17:00
Tuesday 07:30 - 17:00
Wednesday 07:30 - 17:00
Thursday 07:30 - 17:00
Friday 07:30 - 17:00

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Salima District Council posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share